2 Chronicles 26:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uziya adakhala wakhate mpaka pa tsiku la kufa kwake. Tsono popeza kuti anali wakhate, ankakhala m'nyumba ya yekha, chifukwa anali atachotsedwa ku Nyumba ya Chauta. Motero Yotamu mwana wake ndiye amene ankayang'anira za ku nyumba ya mfumu, namalamulira anthu am'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Uziya anali ndi khate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye amakhala mʼnyumba ya yekha ngati wakhate, ndipo samalowa mʼNyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndiye amayangʼanira nyumba yaufumu ndipo ankalamulira anthu a mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa ku nyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wace anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.