2 Chronicles 26:23 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Uziya adalondola makoko ake ndipo adamuika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, osati m'manda mwaomo, poti anthu ankati, “Iyeyu ndi wakhate.” Ndipo Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziya analondola makolo ake, ndipo anamuyika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, koma osati mʼmanda mwawomo poti anthu anati, “Iyeyu anali ndi khate.” Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.