2 Chronicles 26:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uziyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziya anali wa zaka 16 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 70. Dzina la amayi ake linali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.