2 Chronicles 26:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina Uziya adakamenyana nkhondo ndi Afilisti, nagwetsa linga la Gati ndi la Yabine ndiponso la Asidodi. Kenaka adamanga mizinda m'dziko la Asidodi ndi kwinanso m'dziko la Afilisti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo anapita kukachita nkhondo ndi Afilisti ndipo anagwetsa makoma a Gati, Yabine ndi Asidodi. Ndipo kenaka anamanganso mizinda ya pafupi ndi Asidodi ndi malo ena pafupi ndi Afilisti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza anaturuka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.