2 Chronicles 27:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, kutsata zonse zimene ankachita Uziya, bambo wake, kupatula kuti sadakaloŵe mwamphamvu ku Nyumba ya Chauta. Koma anthu ankachitabe zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe m'Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga anachitira Uziya abambo ake, kupatula kuti iyeyo sanalowe mʼNyumba ya Yehova. Komabe anthu anapitirira kuchita zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adacitira atate wace Uziya; pokhapo sanalowa m'Kacisi wa Yehova. Koma anthu anacitabe zobvunda.