2 Chronicles 27:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamenyana nkhondo ndi mfumu ya Aamoni, ndipo adaŵagonjetsa Aamoniwo. Nchifukwa chake, chaka choyamba Aamoni aja adapereka makilogramu 3,400 a siliva, matani 1,000 a tirigu, ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni ankalipira kwa Yotamuyo zinthu zonga zomwezo pa chaka chachiŵiri ndi chachitatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yotamu anachita nkhondo ndi mfumu ya Aamoni ndipo anawagonjetsa. Chaka chimenecho Aamoni anapereka makilogalamu 3,400, matani 1,000 a tirigu ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni anabweretsa zinthu zomwezi chaka chachiwiri ndi chachitatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa, Ndi ana a Amoni anamninkha caka comweci matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye caka caciwiri ndi cacitatu comwe.