2 Chronicles 27:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zonse za Yotamu, ndi nkhondo zake zonse ndiponso makhalidwe ake, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi mafumu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Yotamu, kuphatikizapo nkhondo zake zonse ndi zinthu zina zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zace zonse, ndi njira zace, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.