2 Chronicles 28:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵauza kuti, “Musati mubwere nawo kuno akapolowo, poti inuyo mukufuna kuti ife tichimwire Chauta kuwonjezera pa machimo athu amene tili nawo, ndiponso kuwonjezera pa zolakwa zathu. Ndithu kulakwa kwathu nkwakukulu ndipo mkwiyo woopsa uli pa Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutipalamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa machimo athu ndi zopalamula zathu; pakuti tapalamula kwakukulu, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati, “Musabweretse akapolowo kuno, pakuti ife tidzakhala olakwa pamaso pa Yehova. Kodi mukufuna kuwonjezera pa machimo athu ndi kulakwa kwathu? Pakuti zolakwa zathu ndi zambiri kale ndipo mkwiyo wake woopsa uli pa Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutiparamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa macimo athu ndi zoparamula zathu; pakuti taparamula kwakukuru, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israyeli.