2 Chronicles 28:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka anthu amene taŵatchula maina aja, adanyamuka natenga akapolowo. Amene anali maliseche adaŵaveka zovala zimene adaafunkha. Adaŵaveka, naŵapatsa nsapato. Adaŵapatsa zakudya ndi zakumwa. Tsono atanyamula anthu onse ofooka pa abulu, adabwera nawo kwa abale ao ku Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Kenaka adabwerera ku Samariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene atchulidwa mayina aja anatenga akapolowo, ndipo kuchokera pa zolanda ku nkhondo, anawaveka onse amene anali maliseche. Anawapatsa zovala ndi nsapato, chakudya ndi chakumwa ndi mankhwala. Onse amene anali ofowoka anawakweza pa abulu. Choncho anabwera nawo kwa abale awo ku Yeriko, Mzinda wa Migwalangwa, ndipo kenaka anawabweza ku Samariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanyamuka amuna ochulidwa maina, natenga andende, nabveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zobvala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofoka ao onse pa aburu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.