2 Chronicles 28:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afilisti nawonso anali atathira nkhondo mizinda yakuchigwa ndiponso Megebu wa ku Yuda. Ndipo adalanda Betesemesi, Aiyaloni, Gederoti ndiponso Soko pamodzi ndi midzi yake yomwe, Timna pamodzi ndi midzi yake yomwe, ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yake yomwe, nakhazikika komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi milaga yake, ndi Timna ndi milaga yake, ndi Gimizo ndi milaga yake; nakhala iwo komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo nʼkuti Afilisti atathira nkhondo mizinda ya mʼmbali mwa phiri ndi ku Negevi ku Yuda. Iwo analanda mizindayo nakhala ku Beti-Semesi, Ayaloni ndi Gederoti, komanso Soko, Timna ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yawo yozungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kucidikha, ndi ya kumwela kwa Yuda, nalanda Betisemesi, ndi Azaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi miraga yace, ndi Timna ndi miraga yace; nakhala iwo komweko.