2 Chronicles 28:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi Chauta adalitsitsa dziko la Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi, popeza kuti adaaipitsa ku Yuda, ndipo anali wosakhulupirika kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anapeputsa Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi ya Israeli, pakuti analimbikitsa zoyipa ku Yuda ndipo anali munthu wosakhulupirika kwambiri pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova anacepetsa Yuda cifukwa ca Ahazi mfumu ya Israyeli; popeza iye anacita comasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.