2 Chronicles 28:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko imene idamgonjetsayo, ndipo ankati, “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a ku Siriya yaŵathandiza iwowo, ine ndidzapereka nsembe kwa milunguyo kuti indithandizenso ine.” Koma milunguyo idamuwononga pamodzi ndi anthu ake onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisrayeli onse.