2 Chronicles 28:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahazi adasonkhanitsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta, naziphwanyaphwanya. Kenaka adatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, nadzimangira maguwa pa malo ambirimbiri mu Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngodya zilizonse za Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngondya ziri zonse za Yerusalemu.