2 Chronicles 28:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahazi adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sadamuike m'manda enieni a mafumu. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sanamuyike mʼmanda a mafumu a Israeli. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Ahazi anagona ndi makolo ace, namuika m'mudzi wa Yerusalemu; pakuti sanadza naye ku manda a mafumu a Israyeli; ndipo Hezekiya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.