2 Chronicles 28:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wake, adapereka Ahazi kwa mfumu ya ku Siriya, imene idamgonjetsa. Ndipo anthu ambiri adatengedwa ukapolo kupita ku Damasiko. Chauta adamperekanso Ahaziyo kwa mfumu ya ku Israele, imene idamgonjetsa kotheratu pakupha anthu ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wake anamupereka mʼmanja mwa mfumu ya Aramu. Aaramu anamugonjetsa ndipo anagwira ukapolo anthu ake ambiri napita nawo ku Damasiko. Yehova anamuperekanso mʼmanja mwa mfumu ya Israeli, imene inamuzunza ndi kumuphera anthu ake ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova Mulungu wace anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukuru wa anthu ace, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israyeli, amene anamkantha makanthidwe akuru.