2 Chronicles 28:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Peka mwana wa Remaliya adaphako anthu okwanira 120,000 a ku Yuda pa tsiku limodzi, chifukwa iwowo adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Onsewo anali anthu olimba mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limodzi, Peka mwana wa Remaliya anapha asilikali 120,000 mu Yuda chifukwa Yuda anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao.