2 Chronicles 28:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Zikiri, munthu wamphamvu wa ku Efuremu, adapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu, nduna ya ku nyumba ya mfumu, ndiponso Elikana, wachiŵiri mu ulamuliro wa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efuremu anapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zikiri msilikali wa ku Efereimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu woyangʼanira nyumba yaufumu, ndi Elikana wachiwiri kwa mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efraimu anapha Maseya mwana wa mfumu, ndi Azrikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.