2 Chronicles 28:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Israele adagwira ukapolo abale ao a ku Yuda okwanira 200,000, akazi, ana aamuna, ndi ana aakazi. A ku Israelewo adatenganso zofunkha zambiri kubwera nazo ku Samariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana aamuna ndi aakazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anagwira ukapolo abale awo, akazi, ana aamuna ndi ana aakazi okwanira 200,000. Iwo anafunkhanso katundu wambiri amene anapita naye ku Samariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana amuna ndi akazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya,