2 Chronicles 28:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kumeneko kunali mneneri wina wa Chauta dzina lake Odedi. Iye adapita kuti akakumane ndi gulu lankhondo limene lidadza ku Samariya. Adauza anthuwo kuti, “Popeza kuti Chauta, Mulungu wa makolo anu, adaakwiyira anthu a ku Yuda, adapereka Ayudawo kwa inu. Koma inu mwaŵapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lake Odedi; natuluka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lace Odedi; naturuka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.