2 Chronicles 29:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adamlonga ufumu ali wa zaka 25, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Abiya, mwana wa Zekariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Hezekiya analowa ufumu wake ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Abiya mwana wa Zekariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Hezekiya analowa ufumu wace ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la mace ndiye Abiya mwana wa Zekariya.