2 Chronicles 29:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe ndiwo amene adaaloŵa m'katikati mwa Nyumba ya Mulungu kuti akayeretsemo. Adatulutsa zinthu zonse zonyansa zimene adazipeza m'Nyumbamo, m'bwalo la Nyumbayo. Alevi adazitenga zimenezo, nakazitaya ku mtsinje wa Kidroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe analowa m'kati mwake mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, natulutsira kubwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza m'Kachisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuzitulutsira kunja kumtsinje wa Kidroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe analowa m'kati mwace mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, naturutsira ku bwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza m'Kacisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuziturutsira kunja ku mtsinje wa Kedroni.