2 Chronicles 29:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adayamba mwambo wa kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo, mpamene adafika m'khonde la poloŵera m'Nyumba ya Chauta. Tsono adachita mwambo wa kuyeretsa Nyumba ya Chauta ija pa masiku asanu ndi atatu, ndipo adaimaliza pa tsiku la 16 la mwezi woyambawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira kuchipinda cholowera cha nyumba ya Yehova tsiku lachisanu ndi chitatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira ku likole la Yehova tsiku lacisanu ndi citatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi cisanu ndi cimodzi.