2 Chronicles 29:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatha, adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza kuti, “Tayeretsa Nyumba yonse ya Chauta ija, guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso tebulo la buledi wopereka pamaso pa Chauta, pamodzi ndi zipangizo zake zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo analowa m'katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zake zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo analowa m'katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zace zonse.