2 Chronicles 29:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adabwera ndi ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndiponso atonde asanu ndi aŵiri kuti aperekere nsembe yopepesera uchimo, kuperekera banja la mfumu, Nyumba ya Chauta ndi Yuda. Ndipo iyeyo adalamula ansembe, ana a Aaroni, kuti azipereke pa guwa la Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwera nazo ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi anaankhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yauchimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke pa guwa la nsembe la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anabweretsa ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ziwiri monga nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo la ufumu, la malo opatulika ndi Yuda. Tsono mfumu inalamula ansembe, zidzukulu za Aaroni, kuti apereke zimenezi pa guwa lansembe la Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipoanabweranazong'ombe zisanundi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yaucimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke pa guwa la nsembe la Yehova.