2 Chronicles 29:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthuwo adapha ng'ombe zamphongo zija ndipo ansembe adatenga magazi, nawaza pa guwa. Adaphanso nkhosa zamphongo zija, nawaza magazi ake pa guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso anaankhosa aja, nawaza mwazi pa guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthuwo anapha ngʼombe zazimunazo ndipo ansembe anatenga magazi ake ndi kuwawaza pa guwa lansembe, kenaka anapha nkhosa zazimuna zija ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe; anaphanso ana ankhosa aja ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso ana a nkhosawo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe.