2 Chronicles 29:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka ansembe adazipha, napereka magazi ake pa guwa, kuti akhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraele onse, pakuti mfumu idaalamula kuti nsembe yopsereza ndi nsembe zopepesera uchimo zichitike chifukwa cha Aisraele onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi ansembewo anawapha, nachita nsembe yauchimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kuchita chotetezera Aisraele onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yauchimo zikhale za Aisraele onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ansembe anapha mbuzizo ndipo anapereka magazi ake pa guwa, kuti ukhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraeli onse, pakuti mfumu inalamula kuti nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo zichitike chifukwa cha Aisraeli onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ansembewo anawapha, nacita nsembe yaucimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kucita cotetezera Aisrayeli onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yaucimo zikhale za Aisrayeli onse.