2 Chronicles 29:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaika Alevi kuti azikhala ku Nyumba ya Chauta ndi kumaimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, potsata lamulo la Davide ndi la Gadi mneneri wa mfumu, ndiponso la Natani mneneri. Pakuti lamulo limenelo nlochokera kwa Chauta kudzera mwa aneneri ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ace.