2 Chronicles 29:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Hezekiya adati, “Tsopano inu mwadzipereka kuti mugwire ntchito ya Chauta. Idzani pafupi, mubwere nazo nsembe ndi zopereka zothokozera ku Nyumba ya Chauta.” Msonkhanowo udabwera nazo nsembe ndi zopereka zothokozera. Anthu onse amene anali ndi mtima waufulu adabwera ndi nsembe zopsereza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Hezekiya anati, “Inu mwadzipereka tsopano kwa Yehova. Bwerani ndipo mufike ndi nsembe ndi zopereka zachiyamiko ku Nyumba ya Yehova.” Choncho anthu onse anabweretsa nsembe ndi zopereka zachiyamiko, ndipo anthu onse amene anali ofuna mu mtima mwawo anabweretsa nsembe zopsereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika ku nyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.