2 Chronicles 29:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiŵerengero cha nsembe zopsereza zimene msonkhano udabwera nazo ndi ichi: ng'ombe zamphongo 70, nkhosa zamphongo 100, ndi anaankhosa 200. Zonsezi adazipereka ngati nsembe yopsereza kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kuwerenga kwake kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi anaankhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chiwerengero cha nsembe zopsereza chimene anthu onse anabweretsa chinali ngʼombe zazimuna makumi asanu ndi awiri, nkhosa zazimuna 100, ana ankhosa aamuna 200 ndipo zonsezi zinali za nsembe yopsereza kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kuwerenga kwace kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi ana a nkhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.