2 Chronicles 29:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ansembe anali pang'ono, choncho sadathe kusenda nsembe zonse zopserezazo. Motero poyembekeza kuti ansembe onse adziyeretse, Alevi adaŵathandiza mpaka ntchito yonseyo idatha. Aleviwo adaachita changu kupambana ansembe pakudziyeretsa kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha ntchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ansembe anali ochepa kuti asende zonse zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza mpaka ntchito yonse inatha ndipo mpaka ansembe ena atadziyeretsa, pakuti Alevi anachita changu kudziyeretsa kulekana ndi momwe anachitira ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha nchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula.