2 Chronicles 29:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatsekanso zitseko za khonde la poloŵera, nazima nyale. Sadafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika kwa Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anatsekanso pa khomo chipinda cholowera, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anatsekanso pa khomo la likole, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israyeli.