2 Chronicles 29:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Mulungu adaŵapsera mtima anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu. Adaŵasandutsa ochititsa anthu mantha, odabwitsa anthu ndiponso oti anthu aziŵatsonya monga m'mene mukuwoneramu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale chodabwitsa ndi chotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale codabwiza ndi cotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu.

Recommended Reading