2 Chronicles 3:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mapiko a akerubiwo akaŵatambasula, pamodzi ankakwanira mamita asanu ndi anai. Phiko limodzi la kerubi mmodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba. Phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudzana ndi phiko la kerubi mnzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mapiko a akerubi m'litali mwake ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzake mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mapiko a akerubi m'litali mwace ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzace mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.