2 Chronicles 3:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumaso kwake kwa nyumbayo adamangako nsanamira ziŵiri za msinkhu wa mamita 15 ndi theka. Nsanamira iliyonse inali ndi mutu wa mamita aŵiri nkanthu pamwamba pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iliyonse ndiwo mikono isanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu anamangako zipilala ziwiri, zimene zonse pamodzi zinali zotalika mamita khumi ndi asanu ndi theka; chipilala chilichonse chinali ndi mutu woposera mamita awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iri yonse ndiwo mikono isanu.