2 Chronicles 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanga maunyolo okometsera, ofanafana ndi aja a m'kati mwa Nyumba ya Chauta, naŵaika pamwamba pa nsanamirazo. Adapanganso zinthu zonga makangaza zokwanira 100, ndipo adaziika ku maunyolowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napanga maunyolo a m'chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapanga maunyolo olumikizanalumikizana ndipo anawayika pamwamba pa zipilalazo. Anapanganso makangadza 100 ndipo anawalumikiza ku maunyolo aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napanga maunyolo onga a m'moneneramo, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.