2 Chronicles 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanga nsanamirazo kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ina chakumwera, ina chakumpoto. Yakumwerayo adaitchula kuti Yakini, yakumpotoyo Bowazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kachisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzake ku dzanja lamanzere; nalitcha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Bowazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anayimika nsanamirazo kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu, imodzi mbali ya kummwera ndi inayo mbali ya kumpoto. Nsanamira ya kummwera anayitcha Yakini ndipo ya kumpoto anayitcha Bowazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kacisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzace ku dzanja lamanzere; nalicha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Boazi.