2 Chronicles 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipinda chapoloŵera, m'litali mwake chinali cha mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali wa mamita 54. Nyumbayo m'kati mwake adaikuta ndi golide weniweni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54. Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi likole linali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace zana limodzi mphambu makumr awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golidi woona.