2 Chronicles 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipinda chachikulucho adachichinga ndi matabwa amlombwa, nachikuta ndi golide wosalala, ndipo pamakoma adalochapo zithunzi za kanjedza ndi za maunyolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'nyumba yaikulu tsono anatchinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golide wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipinda chachikulu, khoma lake anakhomera matabwa a payini ndipo analikutira ndi golide wabwino ndi kulikongoletsa ndi zithunzi za kanjedza ndi maunyolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'nyumba yaikuru tsono anacinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golidi wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.