2 Chronicles 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adapanga malo opatulika kwambiri. M'litali mwake anali a mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwa nyumbayo. M'mimba mwake analinso a mamita asanu ndi anai. Adakuta malo opatulikawo ndi golide wosalala wokwanira matani makumi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamanga malo opatulika kwambiri, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; naikuta ndi golide wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anamanga Malo Opatulika Kwambiri ndipo mulitali mwake munali mofanana ndi mulifupi mwa Nyumba mamita asanu ndi anayi. Anakuta mʼkati mwake ndi golide wosalala wolemera matani makumi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamanga malo opatulikitsa, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri; naikuta ndi golidi wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.