2 Chronicles 30:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hezekiya adatumiza mau ku Israele konse ndi ku Yuda, ndipo adalembanso makalata kwa Aefuremu ndi kwa Amanase kuti, “Mubwere ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, kudzachita mwambo wa Paska ya Chauta, Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israyeli ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efraimu ndi Manase, kuti abwere ku nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha.