2 Chronicles 30:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho amithenga aja adapita ku mzinda uliwonse m'dziko lonse la Efuremu ndiponso m'dziko lonse la Manase mpaka kukafika ku Zebuloni. Koma anthu ankaŵaseka monyodola nkumaŵalalatira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amtokoma anapitira m'midzi yonse ya dziko la Efuremu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amtokoma anapitira m'midzi m'midzi mwa dziko la Efraimu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.