2 Chronicles 30:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adayambapo kumagwira ntchito, ndipo ku Yerusalemuko adachotsa maguwa operekapo nsembe ndi ena ofukizirapo lubani, nakaŵataya ku chigwa cha Kidroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauka nachotsa maguwa a nsembe okhala m'Yerusalemu, nachotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kidroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauka nacotsa maguwa a nsembe okhala m'Yerusalemu, nacotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kedroni.