2 Chronicles 30:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adapha mwanawankhosa wa Paska pa mwezi wachiŵiri. Choncho ansembe ndi Alevi adachita manyazi, kotero kuti adadziyeretsa, nabwera ndi nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaphera Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi waciwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anacita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza ku nyumba ya Yehova.