2 Chronicles 30:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakhala m'malo mwao potsata lamulo la Mose, munthu wa Mulungu uja. Ansembewo adawaza magazi amene adalandira kwa Alevi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naima m'malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa chilamulo cha Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira kudzanja la Alevi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naima m'malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa cilamulo ca Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira ku dzanja la Alevi.