2 Chronicles 30:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
amene amaika mtima pa kufunafuna Mulungu, Chauta, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti munthuyo sadatsate malamulo onena za kuyeretsedwa koyenera Nyumba ya Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense wakuika mtima wace kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ace, cinkana sanayeretsedwa monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.