2 Chronicles 30:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu a ku Israele amene analipo ku Yerusalemu kuja, adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri, ndipo adasangalala kwambiri. Alevi pamodzi ndi ansembe ankatamanda Chauta tsiku ndi tsiku, akumuimbira ndi mphamvu zao zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele opezeka m'Yerusalemu anachita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli opezeka m'Yerusalemu anacita madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe cacikuru; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoyimbira zakuliritsa kwa Yehova.