2 Chronicles 30:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hezekiya adalankhula moŵalimbitsa mtima Alevi onse ogwira ntchito ya Chauta mwaluso. Choncho anthuwo adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, napereka nsembe zachiyanjano ndi kuthokoza Chauta, Mulungu wa makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika