2 Chronicles 30:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Msonkhano wonse wa ku Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, gulu lonse la anthu amene adaachokera ku Israele, alendo ongokhala nao amene adaachokera ku dziko la Israele, ndiponso alendo ongokhala nao a ku dziko la Yuda, onsewo adakondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala m'Yuda, anakondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wocokera kwa Israyeli, ndi alendo ocokera ku dziko la Israyeli, ndi okhala m'Yuda, anakondwera.