2 Chronicles 30:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zidaatero chifukwa sankatha kuchita Paskayo pa nthaŵi yake, popeza kuti ansembe oyeretsedwa anali osakwanira, ndipo anthu nawonso anali asanasonkhane ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sanakhoze kumchita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikire, ndi anthu sadasonkhane ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sanakhoza kumcita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikira, ndi anthu sadasonkhana ku Yerusalemu.