2 Chronicles 30:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero amithenga adapita ku Israele konse ndi ku Yuda, atatenga makalata a mfumu ndi a nduna zake. Makalatawo ankanena kuti, ‘Inu Aisraele, bwererani kwa Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, kuti Iyeyo abwerenso kwa otsalanu, amene mudapulumuka kwa mafumu a ku Asiriya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono amtokoma anamuka ndi akalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti, “Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono amtokoma anamuka ndi akalata ofuma kwa mfumu ndi akuru ace mwa Israyeli ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israyeli, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isake, ndi Israyeli, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asuri.